UBWINO WAKE !!!
1- Anthu adzakhala ndi mphamvu kulankhula ndi kulimbikitsa umodzi padziko lonse lapansi.Speaking with one voice.
2- Mafumu ndi akuluakulu wose adzapatsidwa ulemu ,ndi mphamvu zawo zotsogolera anthu ndikulambila Mulungu kudzela mumizimu yamakolo.Mumene zinali nthawi ya M bona. (Kapirintiya).
3- Tidzafalitsa ndi kulimbikitsa mtendele pakati pa anthu padziko lonse.
4- Tidzabwezeletsa ndi kusamalila zankhalango ndizachilengedwe zonse paziko lapansi mokomela anthu akudera limenero.Anthu adzayenda ndikuwona wokha m’mene nkhalango yawonongekela Kukan’goma moyang’ana kumusewu wa Salima ndiku Nkhoma.Tinalola kupembeza malamulo adzachuma za chilombo chomwe chikuwononga nkhalango kuyambila nthawi yatsamunda.Magetsi ndi madzi akanayenera kukhala aulere mwina wotsika mitengo kwambiri.Mwina ndalama zimene a kampani amenewa amatolera gawo lalikulu akanakonzera zakhalango.
5- Anyamata ndi atsikana adzamphunzitsidwa ulemu,kumvera,mwambo wamakolo ,kulimbikira ntchito zotukula miyoyo yawo ndi dziko m’mene zinali nthawi yaka Kamuzu Banda.
6- Anthu adzaphunzitsidwa ubwino woyendetsa zachuma ndi malonda kudzera mumphamvu za mafumu chifukwa ndiwo eni ache dziko ndipo adzakhala mpaka kalekale.
7- Anthu adzaphunzisidwa kuipa kolowa mipingo yomwe cholinga chawo nkubweretsanso utsamunda,ukapolo,umphawi pakati pathu.Kumbukilani mbiri yanu kumbuyoku.Ukapolo waku Afrika ,ku Jamaica,Ku Cuba,ku South Amerika,Ku Noth Amerika ,Ku Ulaya ,Ku Asia.
8- Tidzaunika migwirizano yimene mafumu anasainilana ndi azungu mumbuyomu chifukwa malo sagulitsa koma kubwereketsa ndipo mafumu ndi anthu awo anaphindulanji kufika lero.Mafumu anali kuganiza kuti 99 years ndichaka chimodzi chokha chobzala kenaka malo kuwatsiyira eni ake mafumuwo.Kumbukani mbiri ya John Chilebwe.
9- Anthu adzapasidwa ufulu wawo wachibadwidwe kudziwa mbiri yawo yowona padziko pano osati yonama yimene timakolowekedwa nawoyi.Kodi ku Ulaya ,ku Israel,ku Asia ku Australia anthu akuda analiko ndipo aliko?
10- Thano,ndagi,miyambo yamakolo,nyimbo zamtundu wathu,magule amakolo monga vimbuza,gulewankulu,chimutali ndi zina zotere zizakhala zokometsera Mupingowu.
11- Azimayi achizungu ndi achimwenye azamasulidwa kusinga za malamulo a nsanje a azibambo achizungu ndi achimwenye womwe anakhazikitsa kukaniza azimayiwo kuti akwatirane ndi azibambo achikuda.Akatenga mimba kuchoka kumuzibambo wakuda amamulimbikitsa kuti akaphe mwina kuchotsa mimbayo.Ili ndi tsakho lalikulu pakati pathu.Ubwino wake azimayiwo amadziwa kuti amuna achikuda ali ndi mphamvu kwambiri kuposa azungu mwina amwenye.Chifukwa chake azungu anakhazikitsa zipatala zochotsa mimba maka za ana akuda.Tikambirana nawo azimayiwo zaubwino wosunga ana wotele.Tithokoze amayi ake a Barrack Obama chifukwa chokoma mtima pomusala mwanayo,amene ali President waku Amerika.Ana wotele amakhala ndi nzeru zakuya.Zikomo azimayi achikuda chifukwa simutengapo gawo limenelo.
12- Tizayendera Kalenda wogwirizana ndi nzanyengo m’mene dzuwa limayendera osati kalenda imene yilipoyi.Yikusokoneza kukonzekela(Planning).Zikusonyeza kuti kuyamba kwa chaka kwatu kuno ndi 1 June.Kutha kwa chaka 31 May.Mukati mwa nthawi yamvula simuyenera kukhala mphwando lina lililonse.Kumeneko nkusokoneza ntchito zaulimi ndi zina zotere.
13- Mupingowu udzakhala ndi mphamvu zochula maina azithu mogwirinazana ndi dera ,ndichikhalidwe chakumeneko pa dziko lapansi.
14- Mpingo udzatumidza aneneri kudziko lonse lapansi kukonza zipembezo kuti zikhale muchimake mumene eni akefe tinakhadzikitsira.Mtendere(Peace Mission).
Zikomo kwambiri chifukwa chifukwa cha support yanu imene mumapanga anthu nose kuti titulutse fundozi.Izi zikusonyeza umodzi wathu umene ulipo. Ngati pali zina tumizani kuti tiwonjezere.ku
GLOBAL ORIGINAL CHURCH MPINGO WAMAKOLO
Cell: 0888852590/0995754866
Email:renainssanceafrica@gmail.com